"LIGI YA CHIPIKU IYAMBA PA 28 APRIL" - CRFA
Bungwe loyendetsa mpira mchigawo chapakati ya Central Region Football Association lati ligi ya chaka chino ya Chipiku Stores Central Region Football iyamba pa 28 April chaka chino.
Mlembi wamkulu wa bungweli, Austin Ajawa, watsimikiza za nkhaniyi ndipo wati chilichonse chokhudza ligiyi chili mchimake. Iye watsimikizanso kuti mkumano waukulu wa bungweli uliko kumathero a sabatayi.
"Mkumanowu utithandizira kuunikira mmene chaka chatha tinayendera ndikuti tikonze zonse zolakwika zomwe zinachitika nde tipemphe akuluakulu a matimu onse kuti afike ku mkumanowu." Anatero Ajawa.
Ligiyi ikhale ligi yachiwiri ya mchigawo kuti iyamba pomwe yakummwera iyamba pa 20 April 2024 pomwe yakumpoto iyamba mwezi wa mawa.
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores