"KADONA STARS NDI MMBELWA WARRIORS SANALEMBETSE" - NYASULU
Bungwe loyendetsa mpira mchigawo chakumpoto ya Northern Region Football Association yadandaula kuti matimu akuluakulu omwe amasewera kale mu ligi ya SIMSO and Innobuild Northern Region Football Association atha osapezeka kamba koti sanapezeke.
Mlembi wamkulu wa bungweli, Masiya Nyasulu, watsimikiza kuti chilichonse chili mchimake ndipo ligiyi ikhale ikuyamba pa 4 May 2024 koma matimu ena akuluakulu sanalembetse.
"Zokonzekera zonse zili mchimake ndipo matimu ambiri anaonetsa chidwi chosewera mu ligiyi. Timafuna titakhala ndi matimu 25 kapena 26 koma ambiri alembetsadi koma ena oti amasewera kale mu ligiyi sanalembetse monga Kadona Stars ndi Mmbelwa Warriors sanatero ngakhale kuti kulembetsa tinatseka." Anatero Nyasulu.
Iye wati anthu ayembekezere mpikisano wapamwamba muligiyi pomwe matimu akhale akukonzera za ligiyi.
Ligiyi tsopano ya kwa zaka ziwiri yalowetsa matimu mu ligi yaikulu ya dziko lino opanda kutuluka kamba ka k
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores