"SILVER INALI TIMU YAKUMALOTO KWANGA" - CHIKOOKA
Goloboyi yemwe timu ya Silver Strikers yangosaina kumene, George Chikooka, wati linali khumbo lake kudzasewerako timu ngati Silver Strikers ndikuti agwira ntchito molimbikira.
Iye amayankhula atasaina mgwirizano wake wa zaka zitatu ndi timuyi kutsatira kuchoka kutimu ya Chitipa ndipo wati palibenso chilendo chilichonse chomwe ataone ku Silver Strikers.
"Ndine wokondwa pobwera kutimuyi, anali maloto anga ntadzasewerako kutimuyi ndipo ndingoyamika Mulungu pokwanilitsa malotowa. Palibenso chilendo chilichonse chomwe ndingaone, enawa takhala tikusewera nawo nde palibe chilendo." Anatero Chikooka.
Katswiriyu anali mmodzi mwa magoloboyi omwe anachita bwino mu ligi ya chaka chatha pomwe sanagoletsetse mmasewero 12 ndipo alimbirana pa malo oyamba pagolo ndi Charles Thom komanso Pilirani Mapira.
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores