MPONDA NDI MUNTHALI AKUYAMBA NTCHITO LERO
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya FCB Nyasa Big Bullets wakale, Peter Mponda, ndi goloboyi wa Flames, Brighton Munthali, akuyamba ntchito yawo lero pomwe timu ya Black Leopards ikukumana ndi Pretoria Callies mu masewero oyamba a ligi ya Motsepe Foundation Championship ku South Africa.
Mponda anapita kutimuyi ngati wachiwiri kwa mphunzitsi miyezi iwiri yapitayo ndipo anasankha goloboyi wake wakale ku Sure Stream Academy komanso Wizards FC, Munthali, kuti akagwire nayenso ntchito mdzikoli.
Iwo anakapezako osewera wakale wa Wizards, Raffick Namwera, yemwe agwire nayenso ntchito mu ligi ya chaka chino. Timuyi inatuluka chaka chatha koma inagulanso malo ndipo imenyera nkhondo yoti ilowe mu ligi ya DSTV Premiership. Masewero omwe aliko lero ndi awa:
•La Masia 15:00 Upington City •Pretoria Callies 15:00 Black Leopards •Maritzburg United 19:30 Milford FC
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores