Mphunzitsi wa Flames Meck Mwase wati akhala ndi zokonzekera zabwino pamene mawa akhale akusewera ndi timu ya Guinea mu m'masewero awo oyamba kumpikisano wa AFCON.
A Mwase ati aMalawi omwe akunyazitsa komanso kukaikira timuyi adikire mphindi 90 za masewero a mawa.
Ndipo mmodzi wa wosewera a Flames, Khuda Muyaba wati achita chotheka kuti apambane masewero awo ndi Guinea.
Padakali pano osewera 8 sakhala nawo pa masewero-wa kuphatikizapo Gabadinho Mhango komanso Stanley Sanudi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores