NKHANI
Mphunzitsi watimu ya FCB Nyasa Big Bullets Reserve, Enos Chatama, wavomera kuti akhonza kukakhala wachiwiri kwa mphunzitsi watimu yaikulu, Kalisto Pasuwa.
Malingana ndi malipoti a tsamba la Wa Mpira, timuyi tsopano ikumalizitsa zonse zoti itenge mphunzitsiyu abwere kutimu yaikulu.
Ndipo wachiwiri kwa mphunzitsi watimuyi, Michael Ngore yemwe kwawo ndiku Zimbabwe, apitiliza ntchito yowerenga mmene timu yawo komanso matimu ena akusewera.
Litha kukhala ganizo labwino kutengera ndi perfomance ya Mr Chatama ndi mmene ayendera ndi Reserve side since his inauguration ku team, koma nkhawa yanga ili ku team yaing'onoyi kut itha kukhala ngati yaluza kholo mid-way season zimene zingachititsenso timuyi kusachita bwino pokhala kuti ana aku reserve amuzolowera kwambiri Chatama. Pamenepa tikumbukire kwambiri kuti timu yathu yaing'ono ndi supplier wama players abwino kwambiri and even one of the best reserve sides in the country. Ndikanakonda Chatama akanakhala nawobe anawa, ngati ili issue yozikwezera malipiro i would love akanangokambirana ndi Bullets management kuti amukwezere ku reserve konko
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores