Timu ya Mighty Mukuru Wanderers dzulo yachita mgwirizano watsopano ndi kampani ya Mukuru yomwenso ikhale ikuwonjezeranso thandizo la ndalama zomwe yakhala ikupereka ku timuyi.
Mukuru sikhala yokha poti kampani ina ya Ekhaya Farms Foods ikhalanso ikuthandiza timuyi ndipo mgwirizano wa ma kampani awiriwa azipereka thandizo la ndalama zokwana K760 million pachaka.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores