Chitipa United yapeza thandizo lokwana K505 million
Timu ya Chitipa United ikuyenera kukhala ndi moyo wosinthika mu ligi ya chaka chino kutsatira kupeza thandizo kuchokera ku makampani osiyanasiyana lokwana K505 million.
Izi zadziwika pa mwambo waukulu umene timuyi inakonza lachinayi mu boma la Chitipa.
Kampani ya Zambezi Industry ndiyomwe ili wothandiza wamkulu pomwe yaika K250 million ndipo izioneka pa makaka a timuyi ngati The Spirit of Honour mu mgwirizano wa zaka zitatu.
Enanso othandiza ndi a Xbreed Media Group omwe aziyikapo K150 million, a Pro System Tech aziyika K60 million komanso Blantyre Online College K45 million.
Timuyi inaonetsanso makaka omwe azigwiritsa mtchito mu ligi ya chaka chino pa mwambowu.
Timuyi ikukonzekera kusewera mu ligi ya chaka chino pomwe yakhalabe kuchokera mu 2023 pomwe inalowanso mu ligi.
Photo - Chitipa Platform news
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores