BULLETS ILIPIRA K4 MILLION KU FAM
Bungwe la Football Association of Malawi lapeza timu ya FCB Nyasa Big Bullets yolakwa pa milandu yomwe anayitsegulira ndipo ilipira K4 million ku bungweli.
Komiti yokhazikitsa bata ku bungweli lapeza kuti Bullets inalakwa pa milandu yoyambitsa zipolowe, kugwiragwira mmatupi a oyendetsa masewero komanso kulowetsa masewero a mpira kukhala chisokonezo.
Zilango za milandu yonse zikukwana K4 million ndipo chilango China chapita kwa masapota asanu ndi awiri, Chingeni Agumbala, Shaibu Woyera, Trouble Ndikida Kapito, Alick Tsegula, Ganizani Baba, Dyton Bello ndi Fred Sheriff kuti asadzapezekenso ku masewero aliwonse kwa zaka ziwiri.
Bullets yalamulidwanso kuonetsetsa kuti masapotawa asapezekedi ku bwalo la zamasewero.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores