NKHANI
Tate wa timu ya Creck Sporting Club, Apostle Clifford Kawinga, apereka ndalama yokwana K250,000 kwa osewera komanso aphunzitsi a timuyi kutsatira kugonjetsa timu ya FCB Nyasa Big Bulletd.
Timuyi yalengeza za nkhaniyi pa tsambs lawo la mchezo ndipo uku ndi kuthokoza kamba koyichinya Bullets koyamba kenikeni.
George Chaomba anamwetsa chigoli choyamba kenako anamuthandizira Jack Beza pa chigoli chachiwiri kuti apambane 2-0 pa masewerowa ku bwalo la Aubrey Dimba ku Mchinji.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores