BOTOMANI WADYA MTOLIRO WOSAPSA KU CRECK
Wosewera wa kale watimu ya Mighty Wanderers, Misheck Botoman, wachoka kutimu ya Creck Sporting Club komwe anapitako pomwe ligi ya chaka chino imayamba.
Timuyi ndi yomwe yatsimikiza za Kuchoka kwa katswiriyu pomwe mbali zonse zagwirizana zothetsa mgwirizano wawo.
Botoman wasewerako masewero khumi ndi awiri amu ligi komanso amodzi amu chikho koma sanakwanitse kukhazikika mu timu yoyamba ya Creck Sporting Club.
Pakadali pano, komwe alowere sikunadziwike.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores