Silver ikufunitsitsa kuyamba ndi kuwina mchigawo chachiwiri
Timu ya Silver Strikers yati ikufunitsitsa kuti iyambe ndi chipambano mu Chigawo chachiwiri kuti iwapatse mphamvu zoti achite bwino kwambiri mmasewero awo a chigawochi.
Mphunzitsi watimuyi, Peter Mgangira, ndi yemwe amayankhula patsogolo pa masewero awo ndi Mighty Tigers pa bwalo la Kamuzu ndipo wati akudziwa kuti masewero akhale ovuta Koma ayesetsa kuti achite bwino.
"Nthawi zonse tikakumana ndi Tigers sukhala mpira wophweka Koma takumana nawo kwambiri tawaona momwe akusewerera nde tikayesetsa kuti tipambane chifukwa zitipatsa mphamvu kwambiri kuti tizichita bwino." Iye Anafotokoza.
Iye watinso masewerowa aziwagwiritsanso ntchito ngati kukonzekera chikho cha CAF Champions Ligi ndipo aziyesetsa kuti azichita bwino polimbitsa timuyi.
Timuyi ili pa nambala yachitatu mu ligi ndi mapointsi okwana 30 pomwe inapambana masewero asanu ndi atatu, kufanana mphamvu kasanu ndi kamodzi ndi kugonja kamodzi mu ligi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores