Timu ya FCB Nyasa Big Bullets yakakamizika kukachita zokonzekera zawo pa bwalo la sukulu ya Secondary ya Chitipa kamba koti bwalo la Chitipa lakanizidwa kwa iwo ndi khonsolo ya Chitipa.
Timuyi ili mu bomali poti lamulungu inakumana ndi Chilumba Barracks ndipo ikuyembekezeka kukumananso ndi Chitipa United loweruka likudzali.
Zamveka kuti Bullets inakapempha ku khonsoloyi kuti agwiritseko ntchito pa bwaloli Koma khonsoloyi yakana koma lamulo lalikulu lachokera ku Chitipa United.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores