Ekhaya yatenga Joshua Waka
Timu ya Ekhaya FC yatenga goloboyi watimu ya Blue Eagles, Joshua Waka, yemwe akuyembekezeka kusaina mgwirizano wa zaka zitatu ndi timuyi.
Malingana ndi malipoti a tsamba la Wa Mpira, katswiriyu akuyembekezeka kupezeka pa masewero oyamba omwe Ekhaya isewere mu ligi sabata ya mawa.
Ndipo wapampando watimu ya Blue Eagles, Muhammad Ali watsimikiza kuti Waka akuchoka kutimuyi ndipo wamufunira zabwino pamene akukayamba umoyo wina.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores