"Oyimbirawa aziyimbira iliyonse ya Moyale mpaka ikatenge chikho" - Chatama
Mphunzitsi watimu ya Ekhaya FC, Enos Chatama, wati oyimbira pa masewero . wo ndi Moyale Barracks amakondera eni bwalowa ndipo wapempha Football Association of Malawi kumatenga oyimbira a zigawo zina mmasewero ngati amenewa.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonja 2-1 kuti atuluke mu chikho cha FDH Bank koma wati siwokhutira ndi oyimbira angakhale kuti anachinyitsa zigoli zophweka kwambiri.
"Katatu konse tikanatha kupeza penate Koma oyimbira osayimba mwina ndi mmene mpira kumpoto kuno umayimbidwira chonchi mwina iwowa aziyimbira masewero onse a Moyale akatenge chikho." Anatero Chatama.
Ekhaya inatsogola kudzera mwa Hermes Masinja pa mphindi 13 Koma Charles Nkhoma anabwenza pa penate patangodutsa zisanu ndipo Raphael Phiri anamwetsa chopambanira pa mphindi 32.
Zateremu chidwi cha timuyi chipite ku ligi yaikulu ya m'dziko muno pomwe akhale ndi masewero sabata ya mawa.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores