"Akhale masewero ovuta Koma tikufuna kupambana" - Chatama
Mphunzitsi watimu ya Ekhaya FC, Enos Chatama, wati timu yake ikuyang'ana zopeza chipambano pa masewero awo ndi MAFCO koma sizikhala zophweka pakuti akukumana ndi timu yabwino.
Iye amayankhula patsogolo pa masewerowa omwe aliko loweruka pa bwalo la Kamuzu ndipo wati timu yake yakonza zolakwika zomwe anachita ndi Silver Strikers ndipo awonetse kuti achite bwino.
"Takonzekera kwambiri masewerowa ndipo tapuma chifukwa atatha masewero a Silver sitinasewerenso ena nde ndili ndi chikhulupiliro kuti tipambana kuti tichulutse mwayi wathu wodzatsala mu ligi." Anatero Chatama.
Iye wati MAFCO ndi timu yabwino yomwe ngakhale imavutika imadziwa cholinga ndi kuvuta kwa ligi yaikulu pomwe iwo ndi timu yaing'ono komabe ayesetsa kuti asewere mpira wabwino ndi kupambana.
Timuyi ili pa nambala yachisanu mu ligi pomwe ili ndi ma points okwana 23 pa masewero 14 amene yasewera.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores