NKHANI
Timu ya Creck Sporting Club yasankha mtsogoleri watsopano wa osewera yemwe ndi Hardy Ng'andu kulowa mmalo mwa Hadji Wali yemwe watsogolera timuyi kuchokera chaka chatha.
Malingana ndi malipoti a tsamba la Wa Mpira, mphunzitsi watimuyi, Eliya Kananji ndi yemwe wafuna kusinthaku ndipo Ng'andu agwira ntchito ndi Frank Phiri ngati Wachiwiri wake komanso Gift Kadawati ngati wachitatu.
Ndipo timuyi ikuyembekezeka kulekana ndi osewera okwana asanu ndi awiri patsogolo pa kuyamba Chigawo chachiwiri cha ligi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores