"Palibe chimene chawonongekapo" - Mgangira
Mphunzitsi watimu ya Silver Strikers, Peter Mgangira, wati kungolepherana ndi timu sikukutanthauza kuti zinthu zaipa kutimu yake koma kuti zonse zilibwino ndipo masewero ndi ochuluka mu ligi.
Iye amayankhula atatha masewero omwe alepherana 0-0 ndi Mighty Tigers pa bwalo la Silver ndipo wati anali masewero omwe anasewera bwino koma kuti anakanika kupeza zigoli.
Iye wati anasintha nkulowetsa osewera omwe amasewera kwambiri cha kutsogolo kuti akakamize chigoli komabe zinavuta Koma zonse zilitu bwino.
"Sitinganene kuti kungolepheranaku zinthu zaipa ayi, masewero akadalipo ankhaninkhani, tikuyenera timalize Chigawo choyamba kenako tidzayambe chachiwiri. Chilichonse chili bwinobwino palibe chaipa." Anatero Mgangira.
Silver ikadali pa nambala yachitatu mu ligi pomwe ili ndi mapointsi 27 pa masewero 14 omwe yasewera itapambana kasanu ndi kawiri, kulepherana kasanu ndi kamodzi ndi kugonja kamodzi mu ligiyi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores