"Tayang'ana kwambiri pa kugoletsa zigoli" - Ben
Wachiwiri kwa wotsatira kwa mphunzitsi kutimu ya Civil Service United, Charles Ben, wati akuyembekezera kuti masewero awo ndi MAFCO kukhala zigoli zambiri poti aunikira mbali yogoletsa zigoli mu zokonzekera zawo.
Iye amayankhula pa tsogolo pa masewero omwe matimu awiriwa akumane loweruka pa bwalo la Civo ndipo wati timu yake yakonzekera bwino masewerowa ndipo ieza chipambano.
Iye anatinso molalo ndi yapamwamba kwambiri kwa osewera zomwe zikulimbitsa mtima kuti akhoza kuchita bwino mmasewerowa.
"Tayang'ana kwambiri nkhani yogoletsa zigoli, takhala tikuvutika kugoletsa koma mmasewero awa ndikukhulupilira kuti zigoli zikapezeka ndithu." Anatero Ben.
Timuyi ili pa nambala 13 mu ligi ndi mapointsi asanu pa masewero asanu ndi awiri pakuti yapambana kamodzi ndi kufananitsa mphamvu kawiri ndi kugona kanayi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores