"A Malawi tiwapatsa zotsatira zabwino" - Mponda
Wachiwiri kwa mphunzitsi wa timu ya dziko lino, Peter Mponda, wati akudziwa kuti anthu ambiri akufuna ataona timuyi itapeza chipambano ku mpikisano wa chikho cha COSAFA ndipo ayesetsa kuti apereke chipambanochi lachiwiri.
Iye amayankhula patsogolo pa masewero a timuyi ndi Angola omwe ndi otsiriza mu gulu B ya mpikisanowu ndiponso ongokwanilitsa poti Malawi yatuluka kale ku mpikisanowu.
Iye wati timu yake takonza mwambiri omwe amatsalira ndipo ndi Angola timuyi ichita bwino.
"Titagonja ndi Lesotho tinaunikira kuti zikutivuta kumenyera pagolo koma tsopano ndi Namibia tinasewera bwino koma sitinschinye zomwe anthu zikuwapweteka kwambiri nde mawa tiyesetsa kuti tipereke zotsatira zabwino." Anafotokoza Mponda.
Malawi ili pansi pa gulu B la mpikisanowu pomwe ili ndi point imodzi pa masewero awiri omwe yasewera mu mpikisanowu.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores