Malawi ili pa mphambano potuluka kapena kutsalabe
Timu ya dziko lino ya Malawi ikuyenera kuti isagonje mwanjumira iliyonse komanso ipambane mtsiku la lero pomwe ikukumana ndi ya Namibia mu mpikisano wa chikho cha COSAFA ku South Africa.
Timuyi inayamba mwa udyo pomwe inagonjaze 1-0 ndi Lesotho mmasewero awo oyamba kuti ikhale pansi pa gululi koma mwayi wopitilira ukadalipobe pomwe matimu a Namibia ndi Angola anafanana mphamvu mmasewero oyamba.
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimuyi, Peter Mponda, wati timuyi yakonzw momwe inkasowekera pa masewero awo ndi Lesotho ndipo akukhulupilira kuti achita bwino.
"Timayang'ana mofooka kuti timakanikw kulowa mu box mwa adani athu, timasunga mpira inde koma osafika mmalo moti titha kuwapweteka nde takonza zonsezo tikukhulupilira kuti tichita bwino." Iye Anafotokoza.
Timuyi itha osakhalanso ndi mtsogoleri wa osewera, Maxwell Paipi, amene anavulala ndi Lesotho koma Mponda wati iwo anatenga anyamatanso ena abwino oti atha kugwira ntchito.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores