"SINDIKUDZIWA KUTI MWANA AMENEYU WACHOKERA KUTI? NDIWOVOMEREZEKA?" - MPULULA
Mphunzitsi watimu ya Mighty Tigers, Leo Mpulula, walowa nawo mu gulu la aphunzitsi omwe adandaulako ndi kayimbilidwe ka oyimbira ku bwalo la Chitowe pomwe wati oyimbira Idrissah Katola sanayimbire bwino masewero awo.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonja 2-0 ndi timu ya MAFCO masana a lachitatu ndipo wati oyimbirayu wachita ngati sanaphunzire bwino.
"Kuyimbira kosakhala bwino ndipo sindikudziwa kuti mwana ameneyu wachokera kuti? Kodi ndi wovomerezeka kuyimbira ameneyu? Chifukwa watikanira chigoli chabwinobwino, chabwino mchigawo chachiwiri sitinasewere bwino komabe iyeyo watengapo gawo." Anatero Mpulula.
Iye wati timu yake ingobwereranso pa bwalo la zamasewero kuti ikonze mavuto awo ndi kuti aone chitsogolo kuti achite bwanji mu ligi.
Tigers ili pa nambala 12 mu ligi ndi mapointsi okwana 24 pa masewero 21 omwe yasewera.
Oyimbila alelo unenazowona sanachite bwino zawakanika
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores