"TIONA KOMWE TIKATHERE BASI" - MWALWENI
Mphunzitsi watimu ya Baka City, Kondwani Mwalweni, akuoneka kuti wayamba kuvomereza kuti timu yake ituluka mu ligi ya TNM pomwe wati asewerabe masewero awo mpaka awone pomwe atathere.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonja 3-0 ndi timu ya Bangwe All Stars ndipo wati masewerowa anasewera bwino kungoti anapezetsa zigoli zophweka.
Iye anatinso timu yake imalizitsa masewero awo amu ligimu kenako awona mmene atamalizire mu ligi.
"Ifeyo tikadasewerabe masewero athu onse timaliza ndipo tingoona kuti masewero tikamaliza zikhale motani basi." Anatero Mwalweni.
Timuyi ili pa nambala 16 mu ligi pomwe ili ndi mapointsi asanu ndi atatu pa masewero 21 omwe yasewera ndipo yachinya zigoli 9 zokha ndi kuchinyitsa 54.
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores