Bungwe loyendetsa masewero a mpira wa miyendo m'dziko muno la Football Association of Malawi (FAM) latsimikiza ndinso kukhazikitsa masiku, malo komanso ndandanda wa matimu omwe akuyenera kudzakumana mu ndime ya ma semifinals ya mpikitsano wa FDH Bank Cup.
Ndimeyi yomwe imakhala ndi ma timu anayi omwe amakhala akupikitsana idzaseweredwa pa 17 August chaka chino ndipo masewero otsiriza a ndimeyi adzaseweredwa pa 21 August 2024.
Timu ya Blue Eagles idzakumana ndi timu ya Karonga United pa 17 August pa bwalo la masewero la Civo m'nzinda wa Lilongwe.
Pamene masewero otsiriza a ndimeyi adzakhala pakati pa ma timu a Moyale Barracks ndi a katswiri omwe akuteteza chikhochi, a FCB Nyasa Big Bullets pa bwalo la masewero la Bingu.
Wolemba: Yohane M'bwera
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores