MANOMA AKUKHULUPILIRA NKHOMA
Ochemerera atimu ya Mighty Mukuru Wanderers ochuluka akukhulupilira kuti katswiri watimu yawo, Chimwemwe Nkhoma, atha kukonza mavuto omwe ali ku timuyi ndikulowa mmalo mwa Lawrence Chaziya yemwe wapita ku TP Mazembe ku DRC.
Izi zadziwika pomwe pamveka malipoti kuti timuyi yalowa pa msika kuti isake osewera awiri omwe alowe mmalo mwa Chaziya kutimuyi.
Masapotawa ati Nkhoma akhonza kukhala yankho labwino ndipo timuyi isachedwe ndikuononga ndalama pa osewera ena pomwe ena ali nawo kutimuyi.
Katswiriyu sanasewereko angakhale masewero amodzi chibwerereni kutimuyi kuchokera ku Mayamiko Stars.
Nkhoma wasewerako timu ya dziko lino ya Osewera osadutsa zaka 20 ndi osewera ngati Lloyd Aaron, Crispin Mapemba, Chikumbutso Salima, Kelvin Banda komanso Chifundo Mphasi.
Wolemba: Hastings Kasonga 📷: Nkhoma wavala nambala 4.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores