"TINAYIWALA ZA KUGONJA NDI BULLETS" - MWASE
Mphunzitsi watimu ya Mighty Mukuru Wanderers, Meke Mwase, wati timu yake inayiwala kale za kugonja kwawo ndi timu ya FCB Nyasa Big Bullets pomwe anawalimbikitsa osewera ake popita ku Karonga.
Iye amayankhula patsogolo pa masewero awo ndi timu ya Baka City ku Karonga masana a lachinayi ndipo wati akonzeka kuti achite bwino.
"Tinayiwala za kugonja kwa Bullets tinakambirana mmene tinkabwera ku Karonga nde takonzeka kuti na kunoko kokha tichiteko bwino." Anatero Mwase.
Iye watinso timu yake ilibe osewera ovulala pa omwe ayenda nawo pa masewerowa.
Timu ya Wanderers ichepetsa danga lawo pa Silver Strikers kufikira pa mapointsi asanu ndi anayi pomwe ili ndi mapointsi 25 pa masewero 14.
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr 📷: Wanderers media
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores