"CHIGOLI CHOYAMBA INALI OFFSIDE" - YASIN
Mphunzitsi watimu ya Bangwe All Stars, Rodgers Yasin, wati chigoli chomwe anagoletsa FCB Nyasa Big Bullets choyamba chinawafooketsa osewera ake poti chinali chosayenerera kuvomeredwa.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonja 0-2 pa bwalo la Mpira lachitatu ndipo wati timu yake inaphinjika kamba koti Bullets inalandirako thandizo la Oyimbira.
"Palibe panativuta, mutha kuona kuti osewera anayamba bwino, kusewera bwino koma mwina kutayilira mpake tinachinyitsa chigoli choyamba chomwe chinawafooketsa koma mukuona kwaine inali offside." Anatero Yasin.
Iye wati timu yake situluka mu ligi malingana ndi mmene akuonera zinthu mu ligi ndipo mchigawo chachiwiri amenya nkhondo kuti atolere mapointsi ochuluka.
Timuyi ikadali pa nambala 15 mu ligi pomwe yatolera mapointsi asanu ndi anayi (9) okha pa masewero 15 omwe yasewera.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores