"TIKUFUNA TIMALIZE NDI CHIPAMBANO" - KAUNDA
Mphunzitsi watimu ya Karonga United, Oscar Kaunda, wati akufunitsitsa kuti amalize chigawo choyamba ndi chipambano poti mapointsi atatu awathandiza kuti ayime pabwino mu ligi.
Iye amayankhula patsogolo pa masewero awo ndi timu ya Mzuzu City Hammers pa bwalo la Karonga ndipo wati akukhulupilira kuti akhala masewero ovuta poti anagonjetsa posachedwa Hammers mu chikho cha FDH Bank.
"Takonzekera bwino ndipo tikufuna titamaliza chigawo choyamba ndi mapointsi atatu omwe atithandize kwambiri. Abwera movuta kuti adzabwenze pomwe anagonja mu FDH koma Ife takonzekera." Anatero Kaunda.
Iye wati tsopano timuyi ikusintha kusiyana ndi pomwe ankayitenga mmanja mwa Trevor Kajawa ndipo wati tsogolo likuoneka lowala.
Karonga ili pa nambala yachikhumi ndi chimodzi (11) pomwe ili ndi mapointsi okwana 18 pa masewero 14 omwe yasewera.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores