"WANDERERS NDI INA IFE NDI BANGWE" - YASIN
Mphunzitsi watimu ya Bangwe All Stars, Rodgers Yasin, wati timu yake ili ndi ziwanda zomwe FCB Nyasa Big Bullets inawapatsa pomwe anagonja 5-0 mu chikho cha FDH ndipo wati awa ndi masewero ena.
Iye amayankhula patsogolo pa masewero awo ndi Bullets pa bwalo la Mpira lachitatu ndipo wati sakusamala kuti Bullets yagonjetsa Wanderers koma akapitiliza pomwe anasiyira ndi Moyale.
"Wanderers ndi timu ina ifenso ndi timu ina nde sitikusamala kuti achita bwanji ndi Wanderers koma Ife tipita ndipo tiona kuti zikatha motani tikayesetsa kuti pakutha pa masewero tikasimbe lokoma." Anatero Yasin.
Timu ya Bangwe ili pa nambala 15 mu ligi pomwe ili ndi mapointsi asanu ndi anayi (9) pa masewero 14 omwe timuyi yasewera.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores