"TIKUFUNIKA KUWINA KUTI TIMALIZE PABWINO" - KAMWENDO
Mphunzitsi wogwirizira watimu ya Creck Sporting Club, Joseph Kamwendo, wati timu yake ikudziwa kufunikira komaliza ndi chipambano mmasewero omaliza a mchigawo choyamba cha ligi kuti adzapeze poyambira mchigawo chachiwiri.
Iye amayankhula patsogolo pa masewero awo ndi Premier Bet Dedza Dynamos pa bwalo la Civo lachitatu ndipo wati chipambano chikhala chofunikira poti ayang'ana zomaliza pa nambala yachisanu mu ligi.
"Akhala masewero ovuta poti Dedza ndi timu yabwino koma Ife takonza ndipo kupambana kutilimbikitsa poti ndi timu yoti yalowa kumene mu ligi nde kuti timalize pa nambala yachisanu tikhala ndi chilimbikitso kuti mchigawo chachiwiri tidzachite bwino." Anatero Kamwendo.
Iye wati sakupereka phuma kwa osewera ake koma akungowalimbikitsa poti ndi achisodzera nde akungowalimbikitsa kuti azisewera mpira wawo.
Timuyi ili pa nambala yachisanu ndi chiwiri (7) pomwe ili ndi mapointsi 19 pa masewero 14 omwe yasewera.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores