ADAM ATHA OSAPEZEKA MU DERBY
Katswiri watimu ya Mighty Mukuru Wanderers yemwe ali mkamwa mwa anthu, Adam Wallace, atha osapezeka pa masewero omwe timuyi ikumane ndi FCB Nyasa Big Bullets mu FDH Bank kamba koti amadwala.
Mphunzitsi watimuyi, Meke Mwase, ndi yemwe watsimikiza za nkhaniyi ponena kuti Adam akuunikidwa ndi madotolo ngati angapezeke pa masewerowa.
"Padakali pano osewera aliyense alibwino ndipo ndi wokonzeka kusewera masewero amenewa mwina kupatula Wallace Adam yemwe amadwala ndipo akuyang'anidwa ngati angapezeke mmasewerowa." Anafotokoza Mwase.
Pa masewerowa, mphunzitsiyu wati ndi masewero omwe satengera momwe timu ina ilili koma mmene anyamata akuonekera akupereka chilimbikitso kuti akhonza kuchita bwino.
Matimuwa akukumana kachiwiri mu chaka chino pomwe anakumananso mu ligi ya TNM ndipo anafanana mphamvu 1-1 pa bwalo la Kamuzu.
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores