BULLETS YALONJEZA K100,000 KWA ALIYENSE AKAPHA NOMA
Timu ya FCB Nyasa Big Bullets yalonjeza kuti osewera aliyense akalandira K100,000 pompopompo ngati akakwanitse kugonjetsa timu ya Mighty Mukuru Wanderers mu ndime ya matimu 16 ya mpikisano wa mu chikho FDH Bank.
Mkulu watimuyi, a Albert Chigoga, ndi omwe atsimikiza za izi ndipo ati ndalamazi sizili ngati zopereka mphamvu komatu zowathokoza chifukwa masewero amenewa amakhala ofunikira.
"Ngati maukulu atimuyi taganiza zoti ngati mawa anyamatawa agonjetse Wanderers ndekuti pompopompo akalandira K100,000 ngati kuwathokoza pa ntchito imene agwira chifukwa masewerowa ndi aakulu." Anatero Chigoga.
Iye anati zambiri zomwe atachitilidwe osewerawa zidziwika pomwe masewero amenewa atatha ndipo pokhapokha ngati atapambane chifukwa zambiri zakonzedwera osewerawa.
Timu ya FCB Nyasa Big Bullets ndi imene ikuteteza ukatswiri wa chikhochi ndipo ngati ikapambane mmasewero amenewa ndekuti ikafika mu ndime ya matimu asanu ndi atatu a chikhochi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores