"NDI MMENE ANYAMATA AKUCHITIRA MOYALE YAFA" - MPONDA
Mphunzitsi watimu ya Silver Strikers, Peter Mponda, wati akudziwa kuti masewero awo ndi timu ya Moyale Barracks akhale ovuta kwambiri koma ndi mmene anyamata ake alili akapambana masewerowa.
Iye amayankhula pomwe timuyi imanyamuka kulowera ku Mzuzu komwe ikasewere masewerowa ndipo wati timu yake ikayenda ikumachita bwino zomwe zikuwalimbitsa mtima kuti akachitanso bwino.
"Tikudziwa kuti ndi masewero ovuta kukumana ndi Moyale ku Mzuzu koma anyamata anapitanso ku Blantyre tinachita bwino, ku Karonga tinawinanso nde ndi mmene alili ndikukhulupilira kuti titha kukachita bwino mmasewerowa." Anatero Mponda.
Iye wati zikufunikira kuti chigawo choyamba achimalize ndi chipambano kuti atsegulebe mpata waukulu pa matimu ena ndipo wapeza otsatira atimuyi kukhamukira lamulungu pa bwalo la Mzuzu.
Silver ili pa nambala yoyamba mu ligi pomwe sinagonjeko ndipo ili ndi ma pointsi 36 pa masewero 14 omwe yasewera.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores