MAULE NDI MANOMA ASONKHERANA CHITETEZO
Matimu a FCB Nyasa Big Bullets komanso Mighty Mukuru Wanderers akambirana zoti akhwimitse chitetezo pa masewero omwe matimuwa akumane mu chikho cha FDH Bank cholinga choti masewero adzathe bwino.
Izi zadziwika ndi zomwe mkulu wa masapota atimu ya Bullets, Stone Mwamadi, wayankhula kuti chitetezo chidzakhala chikhwima ndipo masapota adzavomereze mmene zidzathere.
"Pa mkumano wathu ndi anzathu a Wanderers tauzana kuti pa stand iliyonse padzakhala achitetezo omwe sadzadziwika ndipo adzatola aliyense ofuna kusokoneza nde tikuyembekeza masewero abwino, wowinayo adzayende basi kumapita kwawo chimodzimodzi oluzayo." Anatero Mwamadi.
Ndipo potsimikizapo, mkulu wa oyimba nyimbo kubwalo la zamasewero wa Mighty Mukuru Wanderers, Yonah Malunga, wati zomwe wanena Mwamadi ndi zomwe anakambiranadi.
"Stone wanena momveka bwino kwambiri, ngati wamva kuwawa utha kunyamuka kukagendera kwanu komwe Ife tikufuna tidzaonere Derby yabwino chifukwa uyu akudwala ndi w
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores