"NDIFE OKHUTIRA NDI MMENE TIMU YACHITIRA" - KAMWENDO
Mphunzitsi wogwirizira watimu ya Creck Sporting Club, Joseph Kamwendo, wati ndi wokhutira ndi mmene timuyi yachitira mu ligi ya TNM mu chaka chawo choyamba ponena kuti ndi timu yaing'ono komabe yakwanitsa kufika mu matimu asanu ndi atatu oyambilira mu ligi.
Iye amayankhula atatha masewero omwe afanana mphamvu ndi Kamuzu Barracks lachitatu masana ndipo wati timu yake inasewera bwino mchigawo choyamba koma achinyitsa zigoli zoti akanatha kuzipewa.
Iye wati mmene yachitira timu yake yoti yangolowa kumene ndi zopereka chilimbikitso poti anthu ambiri sankayipatsa mpata.
"Ndi timu yaing'ono kwambiri poti yangolowa kumene mu ligi koma tinataya mapointsi ena ake oti sitimayenera kuwataya mimba osewerera pakhomo komabe pokhala timu yaing'ono kuthera mu matimu asanu ndi atatu ndi chilimbikitso chachikulu nde ndife okhutira." Anatero Kamwendo.
Timuyi tsopano ili ndi mapointsi okwana makumi awiri (20) pomwe ili pa nambala yachisanu ndi chiw
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores