"ZATHU SIZILI PABWINO TIKUYENERA KUWINA" - KAMWENDO
Mphunzitsi wogwirizira watimu ya Creck Sporting Club, Joseph Kamwendo, wati timu yake ikungoyenera kuti ichite bwino pomwe ikusewera ndi Kamuzu Barracks poti timu yake yagonja masewero awiri otsogozana.
Iye amayankhula patsogolo pa masewerowa omwe aseweredwe pa bwalo la Aubrey Dimba ku Mchinji ndipo wati akudziwa kuti masewero akhala ovuta koma ayesetsa kuti apambane.
"Akhala masewero ovuta kwambiri poti tikusewera ndi timu yabwino koma tikuwadziwa mmene amasewerera anzathuwa nde tiyesetsa chifukwa tikuchoka kogonja ndi Civil komanso Baka City nde tikungoyenera kupambana." Anatero Kamwendo.
Iye anatinso timu yake yakonza kwambiri kutsogolo kwawo pomwe akukwanitsa kusewera bwino koma sakugoletsa.
Timuyi ili pa nambala yachisanu ndi chitatu pomwe ili ndi mapointsi okwana 19 pa masewero 13 omwe yasewera.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores