"GILBERT CHIRWA ANATIWERENGADI" - MPONDA
Mphunzitsi watimu ya Silver Strikers, Peter Mponda, wayamikira mphunzitsi watimu ya FOMO, Gilbert Chirwa, kuti anawagwiradi pofunika a Silver Strikers mpake anavutika kuti apeze chigoli mmasewero awo.
Iye amayankhula atatha masewero omwe apambana 1-0 pa bwalo la Silver ndipo wati timu ya FOMO inawagwira pakhosi koma mwa mwayi kuti anapeza chigoli mmasewerowa.
"Anali masewero ovuta ndipo timuyamikire Gilbert Chirwa anadekhadi ndipo anatiwerenga mmasewerowa, anadziwa kuti sangathe kusewera mpira opanikizana ndi Ife nde amatisiya kuti tizikhala ndi mpira kenako azipanga counter attack nde nthawi ina amaopsadi koma mwamwayi tinapeza chigoli." Anatero Mponda.
Timuyi ili pa nambala yoyamba mu ligi pomwe ili ndi mapointsi okwana 36 pa masewero 14 omwe yasewera mu ligi ya TNM chaka chino.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores