"TIMASEWERA NDI TIMU YOMWE ILIBWINO" - CHIRWA
Mphunzitsi watimu ya FOMO FC, Gilbert Chirwa, wati timu yake inakumana ndi timu yomwe ilibwino kwambiri chaka chino mchifukwa chake yakanika kupeza chipambano koma wayamikira osewera ake kuti wasewera bwino.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonja 1-0 pa ndi timu ya Silver Strikers pa bwalo la Silver ndipo wati timu yake yaonetsa kuti akabweretsa osewera ena olimba ikhala yabwino.
"Zoonadi tasewera bwino koma timasewera ndi timu yomwe ilibwino kwambiri chaka chino, akutsogola mu ligi nde koma anyamata anayesetsa kwambiri kuti achite bwino koma zinativuta anzathu anatigoletsa koma taonetsa kuti tikhala timu yabwino kukabwera osewera ena." Anatero Chirwa.
Timuyi ikadali pa nambala 12 mu ligi pomwe ili ndi mapointsi okwana 14 pa masewero okwana 14 omwe yasewera mu ligi ya TNM.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores