"MPIRA WAMAYINA UNATHA" - CHIMKWITA
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Karonga United, Crespo Chimkwita, wati mpira wamayina unatha koma wapabwalo lazamasewero pomwe wati anawauza osewera ake kuti asaope mayina ku Bullets.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonjetsa timu ya FCB Nyasa Big Bullets 2-1 pa bwalo la Karonga ndipo wati timu yake ikuchita bwino pakhomo pomwe sanagonjeko mu ligi ya chaka chino pakhomo.
"Anali masewero ovuta kwambiri pomwe tinachinyitsa koma tinawalimbikitsa anyamata kuti asafooke ndipo tinagoletsa tisanakapumulire nde chinatipatsa mphamvu nde tinawauza kuti asaope mayina a achina Babatunde ndi ena koma kuti alimbikire." Anatero Chimkwita.
Iye anati chipambanochi chawathandiza kwambiri pomwe tsopano asuntha pa ndandanda wa matimu mu ligi.
Timuyi tsopano yafika pa nambala yachikhumi (10) pomwe ali ndi mapointsi okwana 18 pa masewero 14 omwe yasewera.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores