"SIZACHILENDO KUGOLETSA ZIGOLI ZISANU" - MPONDA
Mphunzitsi watimu ya Silver Strikers, Peter Mponda, wati sizachilendo kuti apambana ndi zigoli zokwana zisanu mu ligi pomwe wati pa masewero onse omwe amasewera ndi a Blue Eagles okha omwe sanagoletse.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonjetsa timu ya Mzuzu City Hammers 5-0 pa bwalo la Silver lachinayi masana ndipo wati timu yake inakwanitsa kusunga mpira kwambiri zomwe zinawathandiza.
"Anali masewero abwino kwambiri mwina sizachilendo kuti tachinya zigoli 5 ndikukhulupilira kuti masewero onse omwe tasewera timakhala tikuchinya mwina ndi a Blue Eagles okha omwe sitinachinye nde tiwayamikire anyamata agwira ntchito yopambana lero." Anatero Mponda.
Iye anatinso kusintha komwe anapanga pa mphindi 30 za masewerowa kunali kungosungira chabe osewera ena ndikupereka mwayi kwa osewera ngati Emmanuel Kaunga ndi Chisomo Mpachiks omwe akhalitsa osasewera.
Timuyi yaiponyera kwakuya ligi ya TNM pomwe tsopano ili ndi mapointsi okwana 33 pa ma
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores