"SITINAFUNEKONSO CHATAMA IFE" - MTAYA
Mlembi wamkulu wa timu ya Creck Sporting Club, Aaron Mtaya, wati timu yake sinakumanenso ndi mphunzitsi wina aliyense atamuyimitsa mphunzitsi wawo, Macdonald Mtetemera, ndipo zoti akufuna Enos Chatama ndi mphekesera chabe.
Iye amayankhula pomwe amatsimikiza zakuyimitsidwa kwa Mtetemera kuti timuyi iwunikire mmene iye wachitira mu masewero 13 omwe watsogolera timuyi ndipo kuti afotokoza tsogolo lake bwino lino.
Mtaya wati timuyi yangolemba kalatayo kwa Nginde ndipo palibe zoti apezanako ndi Enos Chatama ngati mmene zamvekera pa masamba a mchezo.
"Ifeyo mmene tamuyimitsa Mtetemera sitinakumanepo ndi mphunzitsi winanso ayi, mmene ndanenera tikhale pansi tiunikire mmene wachitira ndipo iyenso mwini adzafotokoza kenako tidzaone chitsogolo." Anatero Mtaya.
Mtetemera wayimitsidwa atatsogolera timuyi pa masewero 13 mu chaka chawo choyamba mu ligi ya TNM ndipo wapambana masewero asanu, kugonja anayi ndi kufanana mphamvu anayinso pomwe ali pa nambala ya
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores