"TINAWALIMBIKITSA KUTI NDINU TIMU YABWINO" - MWASE
Mphunzitsi watimu ya Mighty Mukuru Wanderers, Meke Mwase, wati anawalimbikitsa osewera atimu yawo kuti ndi abwino komanso ndi timu yabwino zomwe zathandizira kuti ayiwale za kugonja ndi Moyale Barracks ndikugonjetsa Chitipa United.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonjetsa Chitipa 2-0 pa bwalo la Kamuzu lachinayi masana ndipo wati timu yake yasewera bwino kwambiri zomwe zawathandizira kuti achite bwino.
"Tiwayamikire anyamata asewera bwino chifukwa sizophweka kuchokera kogonja kuti mukachite bwino koma analimbikira ndipo tinawauza kuti ndinu timu yabwino ya Osewera abwino komanso tili pakhomo nde tikuyenera kupambana nde anayesetsa mpaka tachitadi bwino." Anatero Mwase.
Iye wati tsopano maso awo ali pa masewero awo ndi timu ya MAFCO omwe adzaseweredwe lamulungu ndipo wati ayesetsa kuti akachite bwino.
Timuyi ikadali pa nambala yachiwiri ndi mapointsi 24 pa masewero 13 omwe yasewera mu ligi.
Noma 2..0
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores