NGINDE ZAVUTA KU CRECK
Timu ya Creck Sporting Club yaimitsa mphunzitsi wawo wamkulu, Macdonald Mtetemera, pantchito yake kutimuyi.
Izi zikuchitika patangopita maola ochepa timuyi itagonja 2-1 ndi timu ya Civil Service United pa bwalo la Civo lachitatu zomwe zachititsa kuti aphonye mwayi wofika pa nambala yachiwiri mu ligiyi.
Timuyi ili pa nambala yachisanu ndi chimodzi (6) mu ligi ndi mapointsi okwana 19 pa masewero 13 pomwe yapambana kasanu, kufanana mphamvu kanayi ndi kugonja kanayinso.
Ndipo wachiwiri kwa mphunzitsi watimuyi, Joseph Kamwendo ndi yemwe atatsogolere timuyi pa masewero omwe atsala nawo kuti amalize chigawo choyamba cha ligiyi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores