"TIMU YOTENGA LIGI IMAPANGA ZOMWE TINACHITA NDI KB" - MPONDA
Mphunzitsi watimu ya Silver Strikers, Peter Mponda, wayamikira osewera ake kuti akuchita bwino kwambiri pa masewero awo pomwe akupanga zomwe timu yofuna kutenga ligi imachita.
Iye amayankhula patsogolo pa masewero awo ndi timu ya Mzuzu City Hammers pa bwalo la Silver ndipo wati zomwe timu yake inachita ndi Kamuzu Barracks ndi zapamwamba koma akuyembekeza masewero ovuta ndi Hammers.
"Ndife osangalala kwambiri kuti tikubwereranso pakhomo pomwe tinasewera kale koma tithokoze masapota athu amatitsatira kulikonseko, tikusewera ndi Mzuzu City Hammers, akhala masewero ovuta poti ikusewera bwino ndipo ikumatenga mapointsi." Anatero Mponda.
Iye wati timu yake iyesetsa kuti izichita bwino pa masewero awo onse ndikuti akufunitsitsa kuti achite bwino muligiyi.
Timuyi ili pamwamba pa ligi pomwe ili ndi mapointsi 30 pa masewero 12 omwe asewera mu ligi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores