"OYIMBIRA WATIKANIRA ZIGOLI ZIWIRI" - KAUNDA
Mphunzitsi watimu ya Karonga United, Oscar Kaunda, wati timu yawo yagonja masewero awo kamba koti oyimbira pa masewerowa sanagwire bwino ntchito yake.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonja 2-0 ndi timu ya MAFCO pa bwalo la Chitowe ndipo iye wati abwerera kuti akakonze mavuto awo omwe anachititsa kuti achinyitse zigoli ziwiri pa masewerowa.
"Tagonja inde koma tikhonza kunena kuti anzathuwa sanali bwino ndipo ntchito yawo sanagwire bwino chifukwa tinali ndi zigoli ziwiri zabwinobwino azikana komanso kalikonse komwe tingapange tikapita kutsogolo amayimba." Anatero Kaunda.
Iye anati abwerera kuti akakonze mavuto omwe awaona kuti mmasewero omwe akubwera kutsogolo kwawo adzachite bwino.
Timuyi ili pa nambala 11 mu ligi pomwe yakwanitsa kutolera mapointsi 16 pa masewero 13 omwe yasewera.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores