"SITINATAYE MTIMA TITACHINYITSA" - CHIDATI
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Civil Service United, Wilson Chidati, wati timu yake sinataye mtima itachinyitsa chigoli mchigawo choyamba chifukwa chake inakwanitsa kupambana masewero awo.
Iye amayankhula atatha masewero omwe anachokera kumbuyo kuti agonjetse timu ya Creck Sporting Club pa bwalo la Civo ndipo iye anati anali masewero ovuta poti anyamata onse ndi odziwana.
"Anali masewero ovuta mmene ndinanenera kale kuti anyamata ndi odziwana koma atatichinya mchigawo choyamba sitinataye mtima tinawauza anyamata kuti alimbikirebe mpaka tinapeza zigoli." Anatero Chidati.
Timu ya Civil tsopano ili ndi mapointsi okwana 16 mu ligi pomwe tsopano ili pa nambala 8 pa masewero 13 omwe yasewera.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores