"CIVIL YATHANDIZIDWA NDI OYIMBIRA" - MTETEMERA
Mphunzitsi watimu ya Creck Sporting Club, Macdonald Mtetemera, wati timu yake simayenera kugonja masewero awo ndi Civil Service United koma chifukwa choti oyimbira wathandizira kuti agonje.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonja 2-1 pa bwalo la Civo ndipo wati timu yake inakanilidwa penate yabwino kenako ndi pomwe Civil imakagoletsa chigoli chawo chachiwiri.
"Tagonja zoonadi tivomereze nde tingobwerera kuti tikakonze mavuto athu. Sindimakonda kuyankhula za oyimbira koma leroli wawathandiza a Civil muone chigoli chachiwiri chija atikanira penate yabwinobwino koma akuwapatsa chigoli nde tikayankhula zimakhala zoipa." Anatero Mtetemera.
Timuyi yatsika kufika pa nambala yachisanu ndi chimodzi (6) mu ligi pomwe ali ndi mapointsi okwana 19 pa masewero 13 omwe yasewera.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores