"KUCHOKA KWA SAVIELI SITIPANIKA KWAMBIRI" - CHIDATI
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Civil Service United, Wilson Chidati, wati kuchoka kwa osewera wawo wakutsogolo, Emmanuel Savieli, sikuti avutika kwambiri poti ali ndi anyamata ena omwe alowe pomwe panali iyeyo.
Chidati amayankhula patsogolo pa masewero awo ndi FCB Nyasa Big Bullets lamulungu pa bwalo la Kamuzu ndipo wati Savieli amathandizana kwambiri ndi anzake ndipo angomusowa ngati munthu.
"Kuchoka kwa Savieli timusowa poti amathandizana kwambiri ndi anzake koma sikuti tipanika kwenikweni chifukwa kuli anyamata ena omwe agwire ntchito yomwe iye amagwira." Anatero Chidati.
Pa masewerowa, iye wati anyamata awo akonzekera bwino masewerowa ndipo ngati akatsatire zomwe mphunzitsi wawo wawauza akachita bwino pa masewerowa.
Timuyi ili pa nambala yachisanu ndi chitatu (8) mu ligi pomwe ili ndi mapointsi okwana 14 pa masewero 11 omwe yasewera.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores