"TIKUYESETSA KUTI TIZICHITA BWINO KOYENDA" - CHIRWA
Mphunzitsi watimu ya FOMO FC, Gilbert Chirwa, wati timu yake ikuyesetsa kuti izikwanitsa kuchita bwino ikasewera koyenda pomwe inabwenza zigoli ziwiri ndi Creck Sporting Club sabata yatha ngakhale kuti anagonja mmapenate.
Iye amayankhula patsogolo pa masewero awo ndi timu ya Karonga United loweruka likudzali ndipo wati timu yake yakonzeka kwambiri kuti ikachite bwino.
"Takonzekera masewerowa ndikudziwa kuti nthawi zambiri tikayenda zikumativuta koma sabata yatha tinayesetsa tinagonja kumapenate nde ku Karonga ndikukudziwa bwino ndingowalimbikitsa kuti akathe kulimbikira kuti tikachite bwino." Anatero Chirwa.
Timu ya FOMO ili pa nambala yachikhumi ndi mapointsi okwana 14 pa masewero 11 omwe yasewera mu ligi ya TNM.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores