"MATIMU AKUSILIRA POMWE TILI IFE" - MPONDA
Mphunzitsi watimu ya Silver Strikers, Peter Mponda, wati ndi chonyadilitsa kwa osewera ake kuti akupita mmasewero achikhumi ndi chiwiri mu ligi asanagonjeko ndipo pomwe ali matimu ambiri akumapasilira.
Iye amayankhula patsogolo pa masewero awo ndi timu ya Kamuzu Barracks lamulungu pa bwalo la Civo ndipo iye wati timu yake ikuyenera kubwereranso kopambana ndipo sinali ntchito yovuta kuti anyamata ake azitolere bwinobwino.
"Akhale masewero ovuta kwambiri kutengera kuti Ife tikuchoka kogonja ndipo KB nayonso inagonja nde pena KB imasewera mpira ogunda komanso imasunga mpira nde adzakhala ovuta kwambiri. Tikuyenera kuti tibwerere kopambana, tikupita masewero a 12 mu ligi sitinagonje nde ndi zonyadilitsa kwa ife, matimu ambiri akusilira pomwe tili Ife nde sizinali zovuta kuwalimbikitsa anyamatawa kuti ayiwale za Blue Eagles." Anatero Mponda.
Timuyi ili pa nambala yoyamba mu ligi pomwe ili ndi mapointsi okwana 29 pa masewero 11 omwe yasewera mu
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores